Ndidalakwa chiyani, kepana ndisiye kuyimba? – wadandaula Temwa

Patangodutsa maola ochepa woyimba wamkazi Tuno atadandaula za kusakondedwa, naye Temwa Gondwe wadandaula zomwezo ndipo akudzifusa kuti ‘Ndili kuti’ pomwe anthu ena awugogodi ayamba kumutoza

Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga nchakuti, mkati mwasabatayi, Temwah yemwe ndimwini wake wa nyimbo ya ‘Mvetsera’ yomwe anaimba limodzi ndi Zeze ndipo chaka chatha yawonongetsa anthu ndalama, anayika pa tsamba lake la fesibuku chithuzi cha mwana wake wa miyezi isanu ndi umodzi.

Apa Temwa yemwe chaka chatha wakokolora mphoto za mnanu kamba ka mayimbidwe ake apamwamba, sanadziwe kuti wadzikodolera anthu onunkha nkamwa omwe monga zimachitira ntchentche zikaona chimbudzi, anakhamukira…