Mayi Easter Gondwe omwe akasumilidwa kuti akhala akunyoza nthiti ya oyimba Zeze Kingston, Dorothy, pa fesibuku, ayima pachulu ndikuuza onse omwe akuwavera chisoni kuti adzililire okha ngakhale zikuveka kuti munthu wina wa chiwiri wakawamang’aliraso.
Izi zikudza pomwe Dorothy yemweso amadziwika ndi dzina loti ‘Cash Madam’, wakamang’ala ku bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe kuti Gondwe wakhala akumunyalapsya komaso kumuchepsya kudzera pa tsamba la fesibuku.
Malinga ndi zikalata za ku bwalo la milandu zomwe Malawi24 yaona, mayi Kingstone adandaula kuti mayi Gondwe akhala akuwapekera nkhani zabodza ndikumazithira nsinjiro…