Kulitu nkhani ku bwalo uku. A Easter Gondwe omwe amatchuka ndi kukamba nkhani pa tsamba lino la Facebook akasumilidwa. Doro wa Zeze ndiye wakamang’ala kuti a Gondwe ndi a ‘hater’ ndipo amamudyola kwabasi. Akufuna abwalo awalipitse.
Malinga ndi zikalata za ku bwalo zomwe Malawi24 yaona, a Dorothy Shonga amene nawonso amaziti ndi celebrity komanso ati socialite akagwada ku bwalo kuti lilange Mayi Gondwe.
Malinga ndi zikalatazi, a Shonga omwe ali pa banja ndi oyimba chamba cha Amapiano Zeze ati Mayi Gondwe akhala akuwanamizira mabodza ofuna kuipitsa mbiri yawo.
“Mwa zina, akhala akuuza anthu kuti ine ndimapanga ma kanema olaula,” atero oyimira milandu Mayi…